BENGO KOMETA TSITSI
Tsiku lina bengo ataona tsitsi lake lakula kwambiri anaganiza zokameta koma ndalama analibe. Ali mnjira analingalira kenako anaitana mwana wina.
Bengo : mwanawe tiye tikamete ulele
Mwana: Tiyeni !
Atafika ku babershop:
Bengo: iwe tandimete mpala
Ometa : okay boss
Atamaliza kumeta Bengo anati mwanawe Khala apa akumete. Atasala pang'ono kumaliza kumeta mwana uja, Bengo amvekere ndikubwera ndimugulire tchipis mwanayu
Ometa: koma mfulumire big
Bengo: just two minutes.
Ometa atamaliza kumeta anati: "kodi bambo ako akagula kutali tchipis eti? Mwana amvekere si abambo anga aja anangonditola panjira kuti tiye tikamete ulele